Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 2:4-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Iye adzaweruza pakati pa akunja, adzadzudzula mitundu yambiri ya anthu; ndipo iwo adzasula malupanga ao akhale zolimira, ndi nthungo zao zikhale anangwape; mtundu sudzanyamula lupanga kumenyana ndi mtundu wina, ndipo sadzaphunziranso nkhondo.

5. Inu a nyumba ya Yakobo, tiyeni, tiyende m'kuwala kwa Yehova.

6. Cifukwa inu mwasiya anthu anu a nyumba ya Yakobo, cifukwa kuti iwo adzazidwa ndi miyambo ya kum'mawa, ndipo ali olaula ngati Afilisti, naomba m'manja ndi ana a acilendo.

7. Dziko lao ladzala siliva ndi golidi, ngakhale cuma cao ncosawerengeka; dziko lao lidzalanso akavalo, ngakhale magareta ao ngosawerengeka.

8. Dziko lao ladzalanso mafano; iwo apembedza nchito ya manja ao ao, imene zala zao zao zinaipanga.

9. Munthu wacabe agwada pansi, ndi munthu wamkuru adzicepetsa, koma musawakhululukire.

10. Lowa m'phanga, bisala m'pfumbi, kucokera pa kuopsya kwa Yehova, ndi pa ulemerero wacifumu wace.

11. Maso a munthu akuyang'anira kumwamba adzatsitsidwa, ndi kudzikweza kwa anthu kudzaweramitsidwa pansi; ndipo Yehova yekha adzakwezedwa tsiku limenelo.

12. Cifukwa padzakhala tsiku la Yehova wa makamu pa zonse zonyada ndi zakudzikuza, ndi pa zonse zotukulidwa; ndipo zidzatsitsidwa;

13. ndi pa mitengo yonse yamkungudza ya Lebano, yaitari ndi yotukulidwa, ndi pa mitengo yonse yathundu ya Basana;

14. ndi pa mapiri onse atari, ndi pa zitunda zonse zotukulidwa;

15. ndi pa nsanja zazitari zonse, ndi pa macemba onse;

16. ndi pa ngalawa zonse za Tarisi, ndi pa zithunzithunzi zonse zokondweretsa.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 2