Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 2:1-4 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Mau amene Yesaya mwana wa Amozi anaona, onena za Yuda ndi Yerusalemu.

2. Ndipo padzakhala masiku otsiriza, kuti phiri la nyumba ya Yehova lidzakhazikika pa nsonga ya mapiri, ndipo lidzakwezedwa pamwamba pa zitunda; mitundu yonse idzasonkhana kumeneko.

3. Ndipo anthu ambiri adzanka, nati, Tiyeni tikwere kunka ku phiri la Yehova, ku nyumba ya Mulungu wa Yakobo; ndipo Iye adzatiphunzitsa za njira zace, ndipo tidzayenda m'mayendedwe ace; cifukwa m'Ziyoni mudzaturuka cilamulo, ndi mau a Yehova kucokera m'Yerusalemu.

4. Iye adzaweruza pakati pa akunja, adzadzudzula mitundu yambiri ya anthu; ndipo iwo adzasula malupanga ao akhale zolimira, ndi nthungo zao zikhale anangwape; mtundu sudzanyamula lupanga kumenyana ndi mtundu wina, ndipo sadzaphunziranso nkhondo.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 2