Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 19:17-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. Ndipo dziko la Yuda lidzaopsa Aigupto, yense wakulichula adzamtembenukira mwamantha, cifukwa ca uphungu wa Yehova wa makamu, aupanga pa dzikolo.

18. Tsiku limenelo padzakhala midzi isanu m'dziko la Aigupto yolankhula cinenero ca Kanani, ndi yolumbira, Pali Yehova wa makamu; wina udzachedwa, Mudzi wa cionongeko.

19. Tsiku limenelo padzakhala guwa la nsembe la Yehova pakati pa dziko la Aigupto, ndi coimiritsa ca Yehova m'malire ace.

20. Ndipo cidzakhala cizindikiro ndi mboni ya Yehova wa makamu m'dziko la Aigupto; pakuti iwo adzalirira kwa Yehova, cifukwa ca osautsa, ndipo Iye adzawatumizira mpulumutsi, ndi wamphamvu, nadzawapulumutsa.

21. Ndipo Yehova adzadziwika kwa Aigupto, ndipo Aaigupto adzadziwa Yehova tsiku limenelo; inde iwo adzapembedzera ndi nsembe ndi zopereka, nadzawindira Yehova ndi kucitadi.

22. Ndipo Yehova adzakantha Aigupto kukantha ndi kuciritsa; ndipo iwo adzabwerera kwa Yehova, ndipo Iye adzapembedzedwa ndi iwo, nadzawaciritsa.

23. Tsiku limenelo padzakhala khwalala locokera m'Aigupto kunka ku Asuri, ndipo M-asuri adzafika ku Aigupto, ndi M-aigupto adzafika ku Asuri, ndipo Aaigupto adzapembedzera pamodzi ndi Aasuri.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 19