Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 15:1-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Katundu wa Moabu.Pakuti usiku umodzi Ara wa ku Moabu wapasuka, nakhala cabe; usiku umodzi Kiri wa Moabu wapasuka, nakhala cabe.

2. Akwera kukacisi, ndi ku Dibo, kumisanje, kukalira; pa Nebo ndi pa Medeba a Moabu pali kulira; pamitu pao ponse pali dazi, ndebvu zonse zametedwa.

3. M'makwalala mwao adzimangira ciguduli m'cuuno, pamwamba pa nyumba zao, ndi m'malo a mabwalo ao, yense akuwa, naliritsa kwambiri.

4. Ndi Hesiboni apfuula zolimba, ndi Eliale; mau ao amveka, ngakhale ku Yahazi; cifukwa cace amuna ankhondo a Moabu apfuula zolimba; moyo wace wanthunthumira m'kati mwace.

5. Mtima wanga upfuula cifukwa ca Moabu: akuru ace athawira ku Zoari, ku Eglatiselisiya; pakuti pa cikweza ca Luhiti akwera alikulira, pakuti m'njira ya Horanaimu akweza mpfuu wa cionongeko.

6. Pakuti pa madzi a Nimirimi padzakhala mabwinja; papeza udzu wafota, msipu watha.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 15