1. Katundu wa Moabu.Pakuti usiku umodzi Ara wa ku Moabu wapasuka, nakhala cabe; usiku umodzi Kiri wa Moabu wapasuka, nakhala cabe.
2. Akwera kukacisi, ndi ku Dibo, kumisanje, kukalira; pa Nebo ndi pa Medeba a Moabu pali kulira; pamitu pao ponse pali dazi, ndebvu zonse zametedwa.
3. M'makwalala mwao adzimangira ciguduli m'cuuno, pamwamba pa nyumba zao, ndi m'malo a mabwalo ao, yense akuwa, naliritsa kwambiri.
4. Ndi Hesiboni apfuula zolimba, ndi Eliale; mau ao amveka, ngakhale ku Yahazi; cifukwa cace amuna ankhondo a Moabu apfuula zolimba; moyo wace wanthunthumira m'kati mwace.