Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 14:9-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Kunsi kwa manda kugwedezeka, cifukwa ca iwe, kukucingamira podza pako; kukuutsira iwe mizimu, ngakhale onse akuru akuru a dziko lapansi; kukweza kucokera m'mipando yao mafumu onse a amitundu.

10. Onse adzabvomera, nadzati kwa iwe, Kodi iwe wakhalanso wopanda mphamvu ngati ife? kodi iwe wafanana nafe?

11. Cifumu cako catsitsidwa kunsi ku manda, ndi phokoso la mingoli yako; mbozi zayalidwa pansi pa iwe, ndi mphukutu zakukuta.

12. Wagwadi kucokera kumwamba, iwe nthanda, mwana wa mbanda kuca! Wagwetsedwa pansi, iwe wolefula amitundu!

13. Ndipo iwe unati mumtima mwako, Ndidzakwera kumwamba, ndidzakweza mpando wanga wacifumu pamwamba pa nyenyezi za Mulungu; ndidzakhala pamwamba pa phiri la khamu, m'malekezero a kumpoto;

14. ndidzakwera pamwamba pa mitambo, ndidzafanana ndi Wam'mwambamwamba.

15. Koma udzatsitsidwa kunsi ku manda, ku malekezero a dzenje.

16. Iwo amene akuona iwe adzayang'anitsitsa iwe, nadzalingalira za iwe, ndi kuti, Kodi uyu ndi munthu amene ananthunthumiritsa dziko lapansi, amene anagwedeza maufumu;

17. amene anapululutsa dziko, napasula midzi yace, amene sanamasula ndende zace, zinke kwao?

18. Mafumu onse a amitundu, onsewo agona m'ulemerero yense kunyumba kwace.

19. Koma iwe watayidwa kunja kwa manda ako, ngati nthambi yonyansa, ngati cobvala ca ophedwa, opyozedwa ndi lupanga, otsikira ku miyala ya dzenje, monga ngati mtembo wopondedwa ndi phazi.

20. Iwe sudzaphatikizidwa pamodzi nao poikidwa, pakuti iwe waononga dziko lako, wapha anthu ako; mbeu ya ocita zoipa sidzachulidwa konse.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 14