Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 14:12-30 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Wagwadi kucokera kumwamba, iwe nthanda, mwana wa mbanda kuca! Wagwetsedwa pansi, iwe wolefula amitundu!

13. Ndipo iwe unati mumtima mwako, Ndidzakwera kumwamba, ndidzakweza mpando wanga wacifumu pamwamba pa nyenyezi za Mulungu; ndidzakhala pamwamba pa phiri la khamu, m'malekezero a kumpoto;

14. ndidzakwera pamwamba pa mitambo, ndidzafanana ndi Wam'mwambamwamba.

15. Koma udzatsitsidwa kunsi ku manda, ku malekezero a dzenje.

16. Iwo amene akuona iwe adzayang'anitsitsa iwe, nadzalingalira za iwe, ndi kuti, Kodi uyu ndi munthu amene ananthunthumiritsa dziko lapansi, amene anagwedeza maufumu;

17. amene anapululutsa dziko, napasula midzi yace, amene sanamasula ndende zace, zinke kwao?

18. Mafumu onse a amitundu, onsewo agona m'ulemerero yense kunyumba kwace.

19. Koma iwe watayidwa kunja kwa manda ako, ngati nthambi yonyansa, ngati cobvala ca ophedwa, opyozedwa ndi lupanga, otsikira ku miyala ya dzenje, monga ngati mtembo wopondedwa ndi phazi.

20. Iwe sudzaphatikizidwa pamodzi nao poikidwa, pakuti iwe waononga dziko lako, wapha anthu ako; mbeu ya ocita zoipa sidzachulidwa konse.

21. Konzani inu popherapo ana ace, cifukwa ca kuipa kwa atate ao; kuti iwo asadzauka ndi kukhala nalo dziko, ndi kudzaza dziko lapansi ndi midzi.

22. Ndipo Ine ndidzawaukira, ati Yehova wa makamu, ndi kuononga ku Babulo dzina ndi otsala, ndi mwana wamwamuna, ndi cidzukulu cacimuna, ati Yehova.

23. Ndidzayesapo pokhala nungu, ndi madziwe a madzi; ndipo ndidzasesapo ndi tsace la cionongeko, ati Yehova wa makamu.

24. Yehova wa makamu walumbira, nati, Ndithu monga ndaganiza, cotero cidzacitidwa; ndipo monga ndapanga uphungu, cotero cidzakhala;

25. kuti Ine ndidzatyola Asuri m'dziko langa, ndi pamwamba pa mapiri anga ndidzawapondereza; pomwepo gori lace lidzacoka pa iwo, ndi katundu wace adzacoka paphuzi pao.

26. Umenewu ndi uphungu wopangira dziko lonse; ndipo ili ndi dzanja lotambasulidwa pa amitundu onse.

27. Pakuti Yehova wa makamu wapanga uphungu, ndani adzauleketsa? ndi dzanja lace latambasulidwa, ndani adzalibweza?

28. Caka cimene mfumu Ahazi anamwalira katundu amene analipo.

29. Usakondwere, lwe Filistia, wonsewe, potyoka ndodo inakumenya; pakuti m'muzu wa njoka mudzaturuka mphiri, ndimo cipatso cace cidzakhala njoka yamoto youluka.

30. Ndi oyamba kubadwa a osauka adzadya, aumphawi nadzagona pansi osatekeseka; ndipo ndidzapha muzu wako ndi njala, ndi otsala ako adzaphedwa.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 14