Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 13:6-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Kuwani inu; pakuti tsiku la Yehova liri pafupi; lidzafika monga cionongeko cocokera kwa Wamphamvuyonse.

7. Cifukwa cace manja onse adzafoka, ndi mitima yonse ya anthu idzasungunuka;

8. ndipo adzaopa; zowawa ndi masauko zidzawagwira; ndipo adzamva zowawa, ngati mkazi wakubala; adzazizwa wina ndi wina; nkhope zao zidzanga malawi a moto.

9. Taonani tsiku la Yehova lidza, lankhanza, ndi mkwiyo ndi kukalipira kwaukali; kupasula dziko, ndi kudzaonongamo akucimwa psiti.

10. Cifukwa nyenyezi za kumwamba ndi makamu ao sizidzawala; dzuwa lidzada m'kuturuka kwace, ndipo mwezi sudzaonetsa kuwala kwace.

11. Ndipo ndidzalanga dziko lapansi, cifukwa ca kuipa kwao, ndi oipa cifukwa ca mphulupulu zao; ndipo ndidzaletsa kudzikuza kwa onyada, ndidzagwetsa kudzikweza kwa oopsya.

12. Ndipo ndidzacepsa anthu koposa golidi, ngakhale anthu koposa golidi weniweni wa ku Ofiri.

13. Cifukwa cace ndidzanthunthumiritsa miyamba, ndipo dziko lapansi lidzagwedezeka kucokera m'malo ace, m'mkwiyo wa Yehova wa makamu, tsiku la mkwiyo wace waukali.

14. Ndipo padzakhala kuti monga mbawala yothamangitsidwa, ndi monga nkhosa zosazisonkhanitsa anthu, adzatembenukira yense kwa anthu ace, nathawira yense ku dziko lace.

15. Onse opezedwa adzapyozedwa, ndi onse ogwidwa adzagwa ndi lupanga.

16. Makanda ao adzatswanyidwe pamaso pao; m'nyumba mwao mudzafunkhidwa, ndi akazi ao adzakakamizidwa.

17. Taonani, ndidzawautsira Amedi, amene sadzasamalira siliva, ngakhale golidi sadzakondwera naye.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 13