Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 11:7-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Ndipo ng'ombe yaikazi ndi cirombo zidzadya pamodzi; ndipo ana ao ang'ono adzagona pansi; ndipo mkango udzadya udzu ngati ng'ombe.

8. Ndipo mwana wakuyamwa adzasewera pa una wa mamba, ndi mwana woleka kuyamwa adzaika dzanja lace m'pfunkha la mphiri.

9. Sizidzaipitsa, sizidzasakaza m'phiri langa lonse loyera, cifukwa kuti dziko lapansi lidzadzala ndi odziwa Yehova, monga mdazi adzaza nyanja.

10. Ndipo padzakhala tsiku lomwelo, kuti muzu wa Jese umene uima ngati mbendera ya mitundu ya anthu, amitundu adzafunafuna uwu; ndipo popuma pace padzakhala ulemerero.

11. Ndipo padzakhala tsiku lomwelo, kuti Ambuye adzabweza kaciwiri ndi dzanja lace anthu ace otsala ocokera ku Asuri, ndi ku Aigupto, ndi ku Patirosi, ndi ku Kusi, ndi ku Elamu, ndi ku Sinara, ndi ku Hamati, ndi ku zisumbu za m'nyanja yamcere.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 11