25. Pakuti patsala kamphindi, ndipo ukali udzathedwa ndi mkwiyo wanga wakuwaononga.
26. Ndipo Yehova wa makamu adzamuutsira cikoti, monga m'kuphedwa kwa Midyani pa thanthwe la Orebu; ndipo cibonga cace cidzakhala pamwamba pa nyanja, ndipo adzaisamula monga anacitira Aigupto,
27. Ndipo padzakhala tsiku lomwelo, kuti katundu wace adzacoka pa phewa lako, ndi gori lace pakhosi pako; ndipo gori lidzathedwa cifukwa ca kudzoza mafuta.
28. Wafika ku Aiati, wapitirira kunka ku Migroni; pa Mikimasi asunga akatundu ace;
29. wapita pampata; wagona pa Geba, Rama anthunthumira; Gibeya wa Sauli wathawa.
30. Pfuula ndi mau ako iwe mwana wamkazi wa Galimu! tamva, iwe Laisa! iwe Anatoti wosauka!
31. Madimena ali wothawathawa; okhala m'Gebimu asonkhanakutiathawe.
32. Lero lomwe adzaima pa Nobu; agwedezera dzanja lace pa phiri la mwana wamkazi wa Ziyoni, phiri la Yerusalemu.
33. Taonani, Ambuye Yehova wa makamu adzasadza nthambi moopsya; ndipo zazitari msinkhu zidzadulidwa, ndipo zazitari zidzagwetsedwa.
34. Ndipo adzadula nkhalango za m'thengo ndi citsulo, ndipo Lebano adzagwa ndi wamphamvu.