Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 1:18-31 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Tiyeni, tsono, tiweruzane, ati Yehova; ngakhale zoipa zanu ziri zofiira, zidzayera ngati matalala; ngakhale ziri zofiira ngati kapezi, zidzakhala ngati ubweya wa nkhosa, woti mbu.

19. Ngati inu muli ofuna ndi omvera, mudzadya zabwino za dziko,

20. koma ngati mukana ndi kupanduka, mudzathedwa ndi lupanga; cifukwa m'kamwa mwa Yehova mwatero.

21. Mudzi wokhulupirika wasanduka wadama! wodzala ciweruzowo! cilungamo cinakhalamo koma tsopano ambanda.

22. Siliva wako wasanduka mphala, vinyo wako wasanganizidwa ndi madzi.

23. Akuru ako apanduka, ali anzao a mbala; onse akonda mitulo, natsata zokometsera mirandu; iwo saweruzira amasiye; ngakhale mlandu wa mkazi wamasiye suwafika.

24. Cifukwa cace Yehova ati, Yehova wa makamu wamphamvu wa Israyeli, Ha! ndidzatonthoza mtima wanga pocotsa ondibvuta, ndi kubwezera cilango adani anga;

25. ndipo ndidzaikanso dzanja langa pa iwe, ndi kukusungunula kukusiyanitsa iwe ndi mphala yako, ndipo ndidzacotsa seta wako wonse:

26. ndidzabweza oweruza ako monga poyamba, ndi aphungu ako monga paciyambi; pambuyo pace udzachedwa Mudzi wolungama, mudzi wokhulupirika.

27. Ziyoni adzaomboledwa ndi ciweruzo, ndi otembenuka mtima ace ndi cilungamo.

28. Koma kupasula kwa olakwa ndi kwa ocimwa kudzakhala kumodzi, ndi iwo amene asiya Yehova adzathedwa.

29. Cifukwa adzakhala ndi manyazi, cifukwa ca mitengo yathundu munaikhumba, ndipo inu mudzagwa nkhope, cifukwa ca minda imene mwaisankha.

30. Cifukwa mudzakhala ngati mtengo wathundu, umene tsamba lace linyala, ngatinso munda wopanda madzi.

31. Ndimo wamphamvu adzakhala ngati cingwe cabwazi, ndi nchito yace ngati nthethe; ndipo zonse zidzayaka moto pamodzi, opanda wozimitsa.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 1