Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 1:1-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. MASOMPHENYA a Yesaya mwana wa Amozi, amene iye anaona, onena za Yuda ndi Yerusalemu, masiku a Uziya, Yotamu, Ahazi, ndi Hezekiya, mafumu a Yuda.

2. Imvani, miyamba inu, chera makutu, iwe dziko lapansi, cifukwa Yehova wanena, Ndakulitsa ndipo ndalera ana, ndipo iwo anandipandukira Ine.

3. Ng'ombe idziwa mwini wace, ndi buru adziwa pomtsekereza: koma Israyeli sadziwa, anthu anga sazindikira.

4. Mtundu wocimwa inu, anthu olemedwa ndi mphulupulu, mbeu yakucita zoipa, ana amene acita moononga, iwo amsiya Yehova, iwo amnyoza Woyera wa Israyeli, iwo adana naye nabwerera m'mbuyo.

5. Nanga bwanji mukali cimenyedwere kuti inu mulikupandukirabe? Mutu wonse ulikudwala, ndi mtima wonse walefuka.

6. Kucokera pansi pa phazi kufikira kumutu m'menemo mulibe cangwiro; koma mabala, ndi mikwingwirima, ndi zironda; sizinapole, ngakhale kumangidwa, ngakhale kupakidwa mafuta.

7. Dziko lanu liri bwinja; midzi yanu yatenthedwa ndi moto; dziko lanu alendo alimkudya pamaso panu; ndipo liri labwinja monga lagubuduzidwa ndi alendo.

8. Ndipo mwana wamkazi wa Ziyoni wasiyidwa ngati citando ca m'munda wamphesa, ngati cilindo ca m'munda wamankhaka, ngati mudzi wozingidwa ndi nkhondo.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 1