25. Ciyambire tsiku limene makolo anu anaturuka m'dziko la Aigupto kufikira lero lino, ndatumiza kwa inu atumiki anga onse, aneneri, tsiku ndi tsiku, kuuka mamawa ndi kuwatumiza iwo;
26. koma sanandimvera Ine, sanacherakhutu lao, koma anaumitsa khosi lao; anaipa koposa makolo ao.
27. Ndipo uzinena kwa iwo mau awa onse, koma sadzakumvera iwe; ndipo udzawaitananso; koma sadzakuyankha iwe.
28. Ndipo udzati kwa iwo, Umene ndi mtundu wosamvera mau a Yehova Mulungu wao, wosalola kulangizidwa, coonadi catha, cadulidwa pakamwa pao.
29. Senga tsitsi lako, iwe Yerusalemu, nulitaye, nukweze maliro pa mapiri oti se; pakuti Yehova wakana ndi kusiya mbadwo umene aukwiyira.
30. Pakuti ana a Yuda anacita coipa pamaso panga, ati Yehova; naika zonyansa zao m'nyumba yochedwa dzina langa, kuti alipitse.
31. Namanga akacisi a ku Tofeti, kuli m'cigwa ca mwana wa Hinomu, kuti atenthe m'moto ana ao amuna ndi akazi; cimene sindinauza iwo, sicinalowa m'mtima mwanga.
32. Cifukwa cace, taonani, masiku alikudza, ati Yehova, ndipo sadzachedwanso Tofeti, kapena Cigwa ca mwana wa Hinomu, koma Cigwa ca Kuphera; pakuti adzataya m'Tofeti, kufikira malo akuikamo adzasowa.
33. Ndipo mitembo ya anthu awa idzakhala zakudya za mbalame za mlengalenga, ndi za zirombo za dziko lapansi; palibe amene adzaziopsa.