Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 7:18-30 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Ana atola nkhuni, atate akoleza moto, akazi akanyanga ufa, kuti aumbe mikate ya mfumu yaikazi ya kumwamba, athirire milungu yina nsembe yothira, kuti autse mkwiyo wanga.

19. Kodi autsa mkwiyo wanga? ati Yehova; kodi sadziutsira okha manyazi a nkhope zao?

20. Cifukwa cace, ati Ambuye Mulungu, Taonani, mkwiyo wanga ndi ukali wanga udzathiridwa pa malo ano, pa anthu, ndi pa nyama, ndi pa mitengo ya m'munda, ndi pa zipatso zapansi; ndipo udzatentha osazima.

21. Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli; Ikani zopereka zopsereza zanu pa nsembe zophera zanu, nimudye nyama.

22. Pakuti sindinanena kwa makolo anu, tsiku lija ndinawaturutsa m'dziko la Aigupto, ngakhale kuwauza nsembe zopsereza kapena zophera;

23. koma cinthu ici ndinawauza, kuti, Mverani mau anga, ndipo ndidzakhala Mulungu wanu, ndipo inu mudzakhala anthu anga; nimuyende m'njira yonse imene ndakuuzani inu, kuti cikukomereni.

24. Koma sanamvera, sanachera khutu, koma anayenda m'upo ndi m'kuuma kwa mtima wao woipa, nabwerera cambuyo osayenda m'tsogolo.

25. Ciyambire tsiku limene makolo anu anaturuka m'dziko la Aigupto kufikira lero lino, ndatumiza kwa inu atumiki anga onse, aneneri, tsiku ndi tsiku, kuuka mamawa ndi kuwatumiza iwo;

26. koma sanandimvera Ine, sanacherakhutu lao, koma anaumitsa khosi lao; anaipa koposa makolo ao.

27. Ndipo uzinena kwa iwo mau awa onse, koma sadzakumvera iwe; ndipo udzawaitananso; koma sadzakuyankha iwe.

28. Ndipo udzati kwa iwo, Umene ndi mtundu wosamvera mau a Yehova Mulungu wao, wosalola kulangizidwa, coonadi catha, cadulidwa pakamwa pao.

29. Senga tsitsi lako, iwe Yerusalemu, nulitaye, nukweze maliro pa mapiri oti se; pakuti Yehova wakana ndi kusiya mbadwo umene aukwiyira.

30. Pakuti ana a Yuda anacita coipa pamaso panga, ati Yehova; naika zonyansa zao m'nyumba yochedwa dzina langa, kuti alipitse.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 7