Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 6:1-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ananu a Benjamini, pulumukani pothawa pakati pa Yerusalemu, ombani lipenga m'Tekoa, kwezani cizindikiro m'Beti-hakeremu; pakuti caoneka coipa coturuka m'mpoto ndi kuononga kwakukulu.

2. Ndidzacotsa mwana wamkazi wa Ziyoni mkazi wokoma ndi wololopoka.

3. Abusa ndi nkhosa zao adzadza kwa iye; adzamanga mahema ao pomzinga iye; adzadya yense pokhala pace.

4. Lalikirani nkhondo yakumenyana ndi iye; ukani, tikwere pakati pa usana. Tsoka kwa ife! pakuti dzuwa lapendeka, mithunzi ya madzulo yatambasuka.

5. Ukani, tiyende usiku, tipasule nyumba zace.

6. Pakuti Yehova wa makamu atero, Dulani mitengo, unjikani nthumbira pomenyana ndi Yerusalemu; mudzi wakudzalangidwa ndi uwu; m'kati mwace modzala nsautso.

7. Monga kasupe aturutsa madzi ace, camweco aturutsa zoipa zace; ciwawa ndi kufunkha zimveka m'kati mwace; pamaso panga masiku onse pali kulira ndi mabala.

8. Ulangizidwe, Yerusalemu, ungakucokere moyo wanga, ndingakuyese iwe bwinja, dziko losakhalamo anthu.

9. Yehova wa makamu atero, Adzakunkha otsalira a Israyeli monga mpesa; bweza dzanja lako monga wakuchera mphesa m'mitanga yace.

10. Ndidzanena ndi yani, ndidzacita mboni kwa yani, kuti amve? Taona khutu lao liri losadulidwa, ndipo sangathe kumva; taona, mau a Yehova awatonzetsa iwo; sakondwera nao.

11. Cifukwa cace ndadzala ndi ukali wa Yehova; ndalema ndi kudzikaniza; tsanulirani pa ana a pabwalo, ndi pa masonkhano a anyamata, pakuti ngakhale mwamuna ndi mkazi wace adzatengedwa, okalamba ndi iye amene acuruka masiku ace.

12. Nyumba zao zidzasanduka za ena, pamodzi ndi minda yao ndi akazi ao; pakuti ndidzatambasula dzanja langa pa okhala m'dziko, ati Yehova.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 6