Ndidzanena ndi yani, ndidzacita mboni kwa yani, kuti amve? Taona khutu lao liri losadulidwa, ndipo sangathe kumva; taona, mau a Yehova awatonzetsa iwo; sakondwera nao.