Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 50:25-39 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

25. Yehova watsegula pa nyumba ya zida zace, ndipo waturutsa zida za mkwiyo wace; pakuti Ambuye Yehova wa makamu, ali ndi nchito m'dziko la Akasidi.

26. Tadzani kudzamenyana ndi iye kucokera ku malekezero ace, tsegulani pa nkhokwe zace; unjikani zace monga miyulu, mumuononge konse; pasatsale kanthu ka pa iye.

27. Iphani ng'ombe zamphongo zace zonse; zitsikire kukaphedwa; tsoka iwo! pakuti tsiku lao lafika, tsiku la kulanga kwao.

28. Mau a iwo akuthawa akupulumuka m'dziko la Babulo, kuti alalikire m'Ziyoni kubwezera cilango kwa Yehova Mulungu wathu, kubwezera cilango cifukwa ca Kacisi wace.

29. Memezani amauta amenyane ndi Babulo, onse amene akoka uta; mummangire iye zitando pomzungulira iye, asapulumuke mmodzi wace yense; mumbwezere iye monga mwa nchito yace; monga mwa zonse wazicita, mumcitire iye; pakuti anamnyadira Yehova, Woyera wa Israyeli.

30. Cifukwa cace anyamata ace adzagwa m'miseu yace, ndi anthu ankhondo ace onse adzatontholetsedwa tsiku lomwelo, ati Yehova.

31. Taonani, nditsutsana nawe, wonyada iwe, ati Ambuye, Yehova wa makamu; pakuti tsiku lako lafika, nthawi imene ndidzakulanga iwe.

32. Ndipo wonyadayo adzakhumudwa nadzagwa, ndipo palibe amene adzamuutsa iye; ndipo Ine ndidzayatsa moto m'midzi yace, ndipo udzatentha onse akumzungulira iye.

33. Yehova wa makamu atero: Ana a Israyeli ndi ana a Yuda asautsidwa pamodzi; ndipo onse amene anawagwira ndende awagwiritsitsa; akana kuwamasula.

34. Mombolo wao ngwa mphamvu; dzina lace Yehova wa makamu: adzawanenera mlandu wao ndithu; kuti apumitse dziko lapansi, nadzidzimutse okhala m'Babulo.

35. Lupanga liri pa Akasidi, ati Yehova, pa okhala m'Babulo, pa akuru ace, ndi pa anzeru ace.

36. Lupanga liri pa amatukutuku, ndipo adzapusa; lupanga liri pa anthu olimba ace, ndipo adzaopa.

37. Lupanga liri pa akavalo ao, ndi pa magareta ao, ndi pa anthu onse osanganizidwa amene ali pakati pace, ndipo adzakhala ngati akazi; lupanga liri pa cuma cace, ndipo cidzalandidwa.

38. Cirala ciri pa madzi ace, ndipo adzaphwa; pakuti ndi dziko la mafano osema, ndipo ayaruka ndi kufuna zoopsa.

39. Cifukwa cace zirombo za kucipululu ndi mimbulu zidzakhalamo, ndi nthiwatiwa zidzakhala m'menemo; ndipo sadzakhalamo anthu konse; ndipo sadzakhalamo m'mibadwo mibadwo.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 50