Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 48:3-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Mau amveka kucokera ku Horonaimu, kufunkha ndi kuononga kwakukuru!

4. Moabu waonongedwa; ang'ono ace amveketsa kulira.

5. Pakuti adzakwera pa cikweza ca Luhiti ndi kulira kosaleka; pakuti pa citsiko ca Horonaimu amva kulira kowawa kwa cionongeko.

6. Thawani, pulumutsani miyoyo yanu, mukhale amarisece m'cipululu,

7. Pakuti, cifukwa wakhulupirira nchito zanu ndi cuma canu, iwenso udzagwidwa; ndipo Kemosi adza kundende, ansembe ace ndi akuru ace pamodzi.

8. Ndipo wakufunkha adzafikira pa midzi yonse, sudzapulumuka mudzi uli wonse; cigwa comwe cidzasakazidwa, ndipo cidikha cidzaonongedwa; monga wanena Yehova.

9. Patsani Moabu mapiko, kuti athawe apulumuke; midzi yace ikhale bwinja, lopanda wokhalamo.

10. Atembereredwe iye amene agwira nchito ya Yehova monyenga, atembereredwe iye amene abweza lupanga lace kumwazi.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 48