2. Yehova Mulungu wa Israyeli atero kwa inu, Baruki:
3. Munati, Kalanga ine tsopano! pakuti Yehova waonjezera cisoni pa zowawa zanga; ndalema ndi kubuula kwanga, sindipeza kupuma,
4. Uzitero naye, Yehova atero: Taonani, cimene ndamanga ndidzapasula, ndi cimene ndaoka ndidzazula; ndidzatero m'dziko lonseli.