Mitu

  1. 1
  2. 2
  3. 3
  4. 4
  5. 5
  6. 6
  7. 7
  8. 8
  9. 9
  10. 10
  11. 11
  12. 12
  13. 13
  14. 14
  15. 15
  16. 16
  17. 17
  18. 18
  19. 19
  20. 20
  21. 21
  22. 22
  23. 23
  24. 24
  25. 25
  26. 26
  27. 27
  28. 28
  29. 29
  30. 30
  31. 31
  32. 32
  33. 33
  34. 34
  35. 35
  36. 36
  37. 37
  38. 38
  39. 39
  40. 40
  41. 41
  42. 42
  43. 43
  44. 44
  45. 45
  46. 46
  47. 47
  48. 48
  49. 49
  50. 50
  51. 51
  52. 52

Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 45 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

Mau a Mulungu kwa Baruki

1. Mau amene ananena Yeremiya mneneri kwa Baruki mwana wace wa Neriya, pamene analemba mau awa m'buku ponena Yeremiya, caka cacinai ca Yehoyakimu mwana wace wa Yosiya, mfumu ya Yuda, ndi kuti,

2. Yehova Mulungu wa Israyeli atero kwa inu, Baruki:

3. Munati, Kalanga ine tsopano! pakuti Yehova waonjezera cisoni pa zowawa zanga; ndalema ndi kubuula kwanga, sindipeza kupuma,

4. Uzitero naye, Yehova atero: Taonani, cimene ndamanga ndidzapasula, ndi cimene ndaoka ndidzazula; ndidzatero m'dziko lonseli.

5. Kodi udzifunira wekha zinthu zazikuru? usazifune; pakuti, taona, ndidzatengera zoipa pa anthu onse, ati Yehova: koma moyo wako ndidzakupatsa iwe ngati cofunkha m'malo monse m'mene mupitamo.