Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 4:3-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Pakuti Yehova atero kwa anthu a Yuda ndi kwa Yerusalemu, Limani masala anu, musabzale paminga.

4. Mudzidulire nokha kwa Yehova, cotsani khungu la mitima yanu, amuna inu a Yuda ndi okhala m'Yerusalemu; ukali wanga ungaturuke ngati moto, ungatenthe kuti sangathe kuuzima, cifukwa ca kuipa kwa macitidwe anu.

5. Nenani m'Yuda, lalikirani m'Yerusalemu, ndi kuti, Ombani lipenga m'dzikomo; pfuulani, ndi kuti, Sonkhanani pamodzi, tilowe m'midzi ya malinga.

6. Kwezani mbendera kuyang'ana ku Ziyoni; thawani kuti mupulumuke, musakhale; pakuti ndidza ndi coipa cocokera kumpoto ndi kuononga kwakukuru.

7. Mkango wakwera kuturuka m'nkhalango mwace, ndipo woononga amitundu ali panjira, waturuka m'mbuto mwace kuti acititse dziko lako bwinja, kuti midzi yako ipasuke mulibenso wokhalamo.

8. Pamenepo, bvalani ciguduli, lirani ndi kubuula; pakuti mkwiyo wakuopsya wa Yehova sunabwerera pa ife.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 4