Mkango wakwera kuturuka m'nkhalango mwace, ndipo woononga amitundu ali panjira, waturuka m'mbuto mwace kuti acititse dziko lako bwinja, kuti midzi yako ipasuke mulibenso wokhalamo.