Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 4:11-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Pa nthawi yomweyo adzati kwa anthu awa ndi kwa Yerusalemu, Mphepo yotentha yocokera ku mapiri oti se m'cipululu yopita kwa mwana wamkazi wa anthu anga, yosaungula, yosayeretsa;

12. mphepo yolimba yocokera kumeneko idzandifika ine; tsopanonso ndidzaweruza iwo maweruzo.

13. Taonani, adzadza ngati mitambo, ndi magareta ace ngati kabvumvulu; akavalo ace athamanga kopambana mphungu, Tsoka ife! pakuti tapasuka.

14. Iwe Yerusalemu, utsuke mtima wako kucotsa zoipa kuti upulumuke. Maganizo ako acabe agona mwako masiku angati?

15. Pakuti mau anena m'Dani nalalikira nsautso m'phiri la Efraimu:

16. Mukumbutse mitundu ya anthu; taonani, lalikirani Yerusalemu, kuti owazinga ndi nkhondo afumira ku dziko lakutari, nainenera midzi ya Yuda mau ao.

17. Monga adindo a m'munda amzinga iye; cifukwa andipandukira Ine, ati Yehova.

18. Njira yako ndi nchito zako zinakucitira izi; ici ndico coipa cako ndithu; ciri cowawa ndithu, cifikira ku mtima wako.

19. Matumbo anga, matumbo anga! ndipoteka pamtima panga peni peni; mtima wanga sukhala pansi m'kati mwanga; sindithai kutonthola; pakuti wamva, moyo wanga, mau a lipenga, mbiri ya nkhondo.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 4