Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 4:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ngati udzabwera, Israyeli, ati Yehova, udzabwera kwa Ine; ndipo ngati udzacotsa zonyansa zako pamaso panga sudzacotsedwa.

2. Ndipo udzalumbira, Pali Yehova m'zoonadi, m'ciweruziro, ndi m'cilungamo; ndipo mitundu ya anthu idzadzidalitsa mwa Iye, ndipo mwa Iye adzatamandira.

3. Pakuti Yehova atero kwa anthu a Yuda ndi kwa Yerusalemu, Limani masala anu, musabzale paminga.

4. Mudzidulire nokha kwa Yehova, cotsani khungu la mitima yanu, amuna inu a Yuda ndi okhala m'Yerusalemu; ukali wanga ungaturuke ngati moto, ungatenthe kuti sangathe kuuzima, cifukwa ca kuipa kwa macitidwe anu.

5. Nenani m'Yuda, lalikirani m'Yerusalemu, ndi kuti, Ombani lipenga m'dzikomo; pfuulani, ndi kuti, Sonkhanani pamodzi, tilowe m'midzi ya malinga.

6. Kwezani mbendera kuyang'ana ku Ziyoni; thawani kuti mupulumuke, musakhale; pakuti ndidza ndi coipa cocokera kumpoto ndi kuononga kwakukuru.

7. Mkango wakwera kuturuka m'nkhalango mwace, ndipo woononga amitundu ali panjira, waturuka m'mbuto mwace kuti acititse dziko lako bwinja, kuti midzi yako ipasuke mulibenso wokhalamo.

8. Pamenepo, bvalani ciguduli, lirani ndi kubuula; pakuti mkwiyo wakuopsya wa Yehova sunabwerera pa ife.

9. Ndipo padzakhala tsiku lomwelo, ati Yehova, kuti mtima wa mfumu udzatayika, ndi mitima ya akuru; ndipo ansembe adzazizwa, ndi aneneri adzadabwa.

10. Ndipo ndinati, Ha, Yehova Mulungu! ndithu mwanyenga kwambiri anthu awa ndi Yerusalemu, ndi kuti, Mu'dzalandira mtendere; koma lupanga lafikira pamoyo.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 4