Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 38:1-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Sefatiya mwana wa Matani ndi Gedaliya mwana wa Pusuri, ndi Yukali mwana wa Selemiya, ndi Pasuri mwana wa Malikiya, anamva mau amene Yeremiya ananena ndi anthu onse, kuti,

2. Yehova atero, Iye wakukhala m'mudziwu adzafa ndi lupanga, ndi njala, ndi caola; koma iye wakuturukira kunka kwa Akasidi adzakhala ndi moyo, ndipo adzakhala nao moyo wace ngati cofunkha, nadzakhala ndi moyo.

3. Yehova atero, Mudziwu udzapatsidwatu m'dzanja la nkhondo ya mfumu ya ku Babulo, ndipo adzaulanda.

4. Ndipo akuru anati kwa mfumu, Munthu uyu aphedwetu; cifukwa analopetsa manja a anthu a nkhondo otsala m'mudzi uno, ndi manja a anthu onse, pakunena kwa iwo mau otero; pakuti munthu uyu safuna mtendere wa anthu awa, koma nsautso yao.

5. Ndipo mfumu Zedekiya anati, Taonani, ali m'manja mwanu; pakuti mfumu singathe kucita kanthu kotsutsana nanu.

6. Ndipo anatenga Yeremiya, namponya iye m'dzenje la Malikiya mwana wace wa mfumu, limene linali m'bwalo la kaidi; ndipo anamtsitsa Yeremiya ndi zingwe, Koma m'dzenjemo munalibe madzi, koma thope; namira Yeremiya m'thopemo.

7. Ndipo pamene Ebedi-Meleki Mkusi, mdindo, anamva kuti anamuika Yeremiya m'dzenje; mfumu irikukhala pa cipata ca Benjamini;

8. Ebedi-Meleki anaturuka m'nyumba ya mfumu, nanena ndi mfumu, kuti,

9. Mbuyanga mfumu, anthu awa anacita zoipa m'zonse anacitira Yeremiya mneneri, amene anamponya m'dzenje; ndipo afuna kufa m'menemo cifukwa ca njala; pakuti mulibe cakudya cina m'mudzimu.

10. Ndipo mfumu inamuuza Ebedi-Meleki Mkusi, kuti, Tenga anthu makumi atatu, umkweze numturutse Yeremiya mneneri m'dzenjemo, asanafe.

11. Ndipo Ebedi-Meleki anatenga anthuwo, nalowa nao m'nyumba ya mfumu ya pansi pa nyumba ya cuma, natenga m'menemo nsaru zakale zotaya ndi zansanza zobvunda, nazitsitsira ndi zingwe kwa Yeremiya m'dzenjemo.

12. Ndipo Ebedi-Meleki Mkusi anati kwa Yeremiya, Kulungatu zingwe ndi nsaruzi zotaya zakale ndi zansanza ndi kuzikwapatira. Ndipo Yeremiya anacita comweco.

13. Ndipo anamkweza Yeremiya ndi zingwe, namturutsa m'dzenjemo; ndipo Yeremiya anakhalabe m'bwalo la kaidi.

14. Ndipo mfumu Zedekiya anatuma, natntenga Yeremiya mneneri nalowa naye m'khomo lacitatu la nyumba ya Yehova; ndipo mfumu inati kwa Yeremiya, Ndidzakufunsa iwe kanthu; usandibisire ine kanthu.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 38