Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 37:18-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Ndipo Yeremiya anati kwa mfumu Zedekiya, Ndacimwira inu ciani, kapena atumiki anu, kapena anthu awa, kuti mwandiika m'nyumba yandende?

19. Tsopano ali kuti aneneri anu, amene ananenera inu, kuti, Mfumu ya ku Babulo sidzakudzerani inu, kapena dziko lino?

20. Tsopano tamvanitu, mbuyanga mfumu; pembedzero langa ligwe pamaso panu; kuti musandibwezere ku nyumba ya Yonatani mlembi, ndingafe kumeneko.

21. Ndipo Zedekiya mfumu analamula, ndipo anamuika Yeremiya m'bwalo la kaidi, tsiku ndi tsiku, nampatsa mkate wofuma ku mseu wa oumba mikate, mpaka unatha mkate wonse wa m'mudzi. Ndipo Yeremiya anakhala m'bwalo la kaidi.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 37