Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 36:21-26 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

21. Ndipo mfumu anatuma Yehudi atenge mpukutuwo; ndipo anautenga kuturuka nao m'cipinda ca Elisama mlembi, Ndipo Yehudi anauwerenga m'makutu a mfumu, ndi m'makutu a akuru onse amene anaima pambali pa mfumu.

22. Ndipo mfumu anakhala m'nyumba ya nyengo yacisanu mwezi wacisanu ndi cinai; ndipo munali moto m'nkhumbaliro pamaso pace.

23. Ndipo panali, pamene Yehudi anawerenga masamba atatu pena anai, mfumu inawadula ndi kampeni ka mlembi, niwaponya m'moto wa m'nkhumbaliromo, mpaka mpukutu wonse unatha kupsa ndi moto wa m'nkhumbaliromo.

24. Ndipo sanaopa, sanang'ambe nsaru zao, kapena mfumu, kapena atumiki ace ali yense amene anamva mau onsewa.

25. Tsononso Elinatani ndi Deliya ndi Gemariya anapembedzera mfumu kuti asatenthe mpukutuwo; koma anakana kumvera.

26. Ndipo mfumu inauza Yeremeeli mwana wace wa mfumu, ndi Seraya mwana wa Azirieli, ndi Selemiya mwana wa Abidieli, kuti awagwire Baruki mlembi ndi Yeremiya mneneri; koma Yehova anawabisa.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 36