Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 35:3-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Ndipo ndinatenga Yaasaniya mwana wa Yeremiya, mwana wa Habazinya, ndi abale ace, ndi ana amuna ace, ndi nyumba yonse ya Arekabu;

4. ndipo ndinawalowetsa m'nyumba ya Yehova, m'cipinda ca ana a Hanani mwana wa Igadaliya, munthu wa Mulungu, cokhala pambali pa cipinda ca akuru, ndico cosanjika pa cipinda ca Maseya mwana wa Salumu, mdindo wa pakhomo;

5. ndipo ndinaika pamaso pa ana amuna a nyumba ya Arekabu mbale zodzala ndi vinyo, ndi zikho, ndipo ndinati kwa iwo, Imwani vinyo.

6. Koma anati, Sitidzamwa vinyo; pakuti Yonadabu mwana wa Rekabu kholo lathu anatiuza ife, kuti, Musadzamwe vinyo, kapena inu, kapena ana anu, kumuyaya;

7. ndiponso musamange nyumba, musafese mbeu, musaoke mipesa, musakhale nayo; koma masiku anu onse mudzakhale m'mahema; kuti mukhale ndi moyo masiku ambiri m'dziko limene mukhalamo alendo.

8. Ndipo ife tamva mau a Yonadabu mwana wa Rekabu kholo lathu m'zonse zimene anatiuza ife, zakuti tisamwe vinyo masiku athu onse, ife, akazi athu, ana athu amuna ndi akazi;

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 35