Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 33:17-26 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. Pakuti Yehova atero: Davide sadzasowa munthu wokhala pa mpando wacifumu wa nyumba ya Israyeli;

18. ndiponso ansembe sadzasowa munthu pamaso panga wakupereka nsembe zopsereza, ndi kutentha nsembe zaufa, ndi wakucita nsembe masiku onse.

19. Ndipo mau a Yehova anadza kwa Yeremiya, kuti,

20. Ngati mukhoza kuswa pangano langa la usana ndi pangano langa la usiku, kuti usakhalenso usana ndi usiku m'nyengo yao;

21. pamenepo pangano langa lidzasweka ndi Davide mtumiki wanga, kuti asakhale ndi mwana wamwamuna wakulamulira pa mpando wa ufumu wace; ndiponso ndi Alevi ansembe, atumiki anga.

22. Monga khamu la kuthambo silingathe kuwerengedwa, ndi mcenga wa kunyanja sungathe kuyesedwa; comweco ndidzacurukitsa mbeu za Davide mtumiki wanga, ndi Alevi akunditumikira Ine.

23. Ndipo mau a Yehova anadza kwa Yeremiya, kuti,

24. Kodi sulingalira comwe anena anthu awa, kuti, Mabanja awiri amene Yehova anawasankha, wataya iwo? comweco anyoza anthu anga, kuti asakhalenso mtundu pamaso pao.

25. Yehova atero: Likaleka kukhala pangano langa la usana ndi usiku, ngati sindinalemba malemba a kumwamba ndi dziko lapansi;

26. pamenepo ndidzatayanso mbeu ya Yakobo, ndi ya Davide mtumiki wanga, kuti sindidzatenganso za mbeu zace kuti zikhale zolamulira mbeu za Abrahamu, ndi za Isake, ndi za Yakobo; pakuti ndidzabweundende wao, ndipo ndidzawacitira cifundo.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 33