Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 30:18-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Atero Yehova: Taonani, ndidzabwezanso undende wa mahema a Yakobo, ndipo ndidzacitira cifundo zokhalamo zace, ndipo mudzi udzamangidwa pamuunda pace, ndi cinyumba cidzakhala momwe.

19. Ndipo padzaturuka pa izo mayamikiro ndi mau a iwo okondwerera; ndipo ndidzacurukitsa iwo, sadzakhala owerengeka; ndidzawacitiranso ulemu, sadzacepa.

20. Ana aonso adzakhala monga kale, ndipo msonkhano wao udzakhazikika pamaso panga, ndipo ndidzalanga onse amene akupsinja iwo.

21. Ndipo mkuru wao adzakhala mwa iwo, ndi wolamulira wao adzaturuka pakati pao; ndipo ndidzamyandikitsa iye, ndipo adzayandikira kwa Ine, pakuti iye wolimba mtima kuyandikira kwa Ine ndani? ati Yehova.

22. Ndipo inu mudzakhala anthu anga, ndipo ndidzakhala Mulungu wanu.

23. Taonani, cimphepo ca Yehova, kupsya mtima kwace, caturuka, cimphepo cakukokolola: cidzagwa pamtu pa oipa.

24. Mkwiyo waukali wa Yehova sudzabwerera, mpaka wacita, mpaka watha zomwe afuna kucita m'mtima mwace: masiku akumariza mudzacizindikira.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 30