Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 29:14-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Ndipo ndidzapezedwa ndi inu, ati Yehova, ndidzabwezanso undende wanu, ndipo ndidzasonkhanitsa inu kwa mitundu yonse, ndi kumalo konse kumene ndinakupitikitsirani inu, ati Yehova; ndipo ndidzakubwezeraninso kumalo kumene ndinakutengani inu andende.

15. Pakuti mwati, Yehova watiutsira ife aneneri m'Babulo.

16. Pakuti Yehova atero za mfumu imene ikhala pa mpando wacifumu wa Davide, ndi za anthu onse amene akhala m'mudzi uno, abale anu amene sanaturukira pamodzi ndiinu kundende;

17. Yehova wa makamu atero: Taonani, ndidzatuma pa iwo lupanga, ndi njala, ndi caola, ndipo ndidzayesa iwo onga nkhuyu zoola, zosadyeka, pokhala nzoipa.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 29