Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 29:1-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Amenewa ndi mau a kalata uja anatumiza Yeremiya mneneri kucokera ku Yerusalemu kunka kwa akuru otsala a m'nsinga, ndi kwa ansembe, ndi kwa aneneri, ndi kwa anthu onse, amene Nebukadnezara anawatenga ndende ku Yerusalemu kunka ku Babulo;

2. anatero atacoka ku Yerusalemu Yekoniya mfumu ndi amace a mfumu ndi adindo ndi akuru a Yuda ndi a ku Yerusalemu, ndi amisiri, ndi acipala,

3. anatumiza kalatayo m'dzanja la Elasa mwana wace wa Safani, ndi Gemariya mwana wace wa Hilikiya, amene Zedekiya mfumu ya Yuda anawatuma ku Babulo kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babulo, kuti,

4. Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli atero, kwa am'nsinga onse, amene ndinawatenga ndende ku Yerusalemu kunka nao ku Babulo:

5. Mangani nyumba, khalani m'menemo; limani minda, idyani zipatso zace;

6. tengani akazi, balani ana amuna ndi akazi; kwatitsani ana anu amuna, patsani ananu akazi kwa amuna, kuti abale ana amuna ndi akazi; kuti mubalane pamenepo, musacepe.

7. Nimufune mtendere wa mudzi umene ndinakutengerani am'nsinga, nimuwapempherere kwa Yehova; pakuti mwa mtendere wace inunso mudzakhala ndi mtendere.

8. Pakuti Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli atero: Aneneri anu ndi akuombeza anu amene akhala pakati panu, asakunyengeni inu, musamvere maloto anu amene mulotetsa.

9. Pakuti anenera kwa inu zonama m'dzina langa; sindinatuma iwo, ati Yehova.

10. Pakuti Yehova atero, kuti, Zitapita zaka makumi asanu ndi awiri pa Babulo, ndidzakuyang'anirani inu, ndipo ndidzakucitirani inu mau anga abwino, ndi kubwezera inu kumalo kuno.

11. Pakuti ndidziwa malingiriro amene ndilingiririra inu, ati Yehova, malingiriro a mtendere, si a coipa, akukupatsani inu adzukulu ndi ciyembekezero.

12. Pamenepo mudzandiitana Ine, ndipo mudzanka ndi kupemphera kwa Ine, ndipo ndidzakumverani inu.

13. Ndipo mudzandifuna Ine, ndi kundipeza, pamene mundifuna ndi mtima wanu wonse.

14. Ndipo ndidzapezedwa ndi inu, ati Yehova, ndidzabwezanso undende wanu, ndipo ndidzasonkhanitsa inu kwa mitundu yonse, ndi kumalo konse kumene ndinakupitikitsirani inu, ati Yehova; ndipo ndidzakubwezeraninso kumalo kumene ndinakutengani inu andende.

15. Pakuti mwati, Yehova watiutsira ife aneneri m'Babulo.

16. Pakuti Yehova atero za mfumu imene ikhala pa mpando wacifumu wa Davide, ndi za anthu onse amene akhala m'mudzi uno, abale anu amene sanaturukira pamodzi ndiinu kundende;

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 29