Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 28:1-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo panali caka comweco, poyamba Zedekiya kukhala mfumu ya Yuda, caka cacinai, mwezi wacisanu, kuti Hananiya mwana wa Azuri mneneri, amene anali wa ku Gibeoni, ananena ndi ine m'nyumba ya Yehova, pamaso pa ansembe ndi pa anthu onse, kuti,

2. Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli, kuti, Ndatyola gori la mfumu ya ku Babulo.

3. Zisanapite zaka ziwiri zamphumphu Ine ndidzabwezeranso kumalo kuno zipangizo zonse za m'nyumba ya Yehova, zimene Nebukadinezara mfumu ya ku Babulo anazicotsa muno, kunka nazo ku Babulo;

4. ndipo ndidzabwezeranso kumalo kuno Yekoniya mwana wace wa Yehoyakimu, mfumu ya Yuda, ndi am'nsinga onse a Yuda, amene ananka ku Babulo, ati Yehova: pakuti ndidzatyola gori la mfumu ya ku Babulo.

5. Ndipo Yeremiya mneneri anati kwa Hananiya mneneri pamaso pa ansembe, ndi pamaso pa anthu onse amene anaima m'nyumba ya Yehova,

6. Yeremiya mneneri anati, Amen: Yehova acite cotero: Yehova atsimikize mau ako amene wanenera, abwezerenso zipangizo za nyumba ya Yehova, ndi onse amene anacotsedwa am'nsinga, kucokera ku Babulo kudza kumalo kuno.

7. Koma mumvetu mau awa amene ndinena m'makutu anu, ndi m'makutu a anthu onse:

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 28