Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 27:14-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Musamvere mau a aneneri amene anena ndi inu, kuti, simudzamtumikira mfumu ya ku Babulo; pakuti akunenerani zonama.

15. Pakuti sindinawatuma iwo, ati Yehova, koma anenera zonama m'dzina langa; kuti ndikupitikitseni inu, kuti mudzathedwe, inu, ndi aneneri amene anenera kwa inu.

16. Ndiponso ndinanena kwa ansembe ndi kwa anthu onsewa, kuti, Yehova atero: Musamvere mau a aneneri anu amene akunenerani inu, kuti, Taonani, zipangizo za nyumba ya Yehova zidzatengedwanso ku Babulo posacedwa; pakuti akunenerani inu zonama.

17. Musamvere amenewa; mtumikireni mfumu ya ku Babulo, ndipo mudzakhala ndi moyo; cifukwa canji mudzi uwu udzakhala bwinja?

18. Koma ngati ndiwo aneneri, ndipo ngati mau a Yehova ali ndi iwo, tsopano apembedzere Yehova wa makamu, kuti zipangizo zotsala m'nyumba ya Yehova, ndi m'nyumba ya mfumu ya Yuda, ndi ku Yerusalemu, zisanke ku Babulo.

19. Pakuti Yehova wa makamu atero, za zoimiritsa, ndi za thawale, ndi za zoikirapo, ndi za zipangizo zotsala m'mudzi uwu,

20. zimene sanazitenga Nebukadinezara mfumu ya ku Babulo, pamene anamtenga ndende Yekoniya mwana wace wa Yehoyakimu, mfumu ya Yuda, kucokera ku Yerusalemu kunka ku Babulo; ndi akuru onse a Yuda ndi Yerusalemu;

21. inde, atero Yehova, Mulungu wa Israyeli, za zipangizo zotsala m'nyumba ya Yehova, ndi m'nyumba ya mfumu ya Yuda, ndi ku Yerusalemu;

22. adzanka nazo ku Babulo, kumeneko zidzakhala, mpaka tsiku limene ndidzayang'anira iwo, ati Yehova; pamenepo ndidzazikweza, ndi kuzibwezera kumalokuno.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 27