Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 25:14-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Pakuti mitundu yambiri ndi mafumu akuru adzayesa iwo atumiki ao; ndipo ndidzabwezera iwo monga mwa macitidwe ao, monga mwa nchito ya manja ao.

15. Pakuti Yehova, Mulungu wa Israyeli, atero kwa ine, Tenga cikho ca vinyo wa ukaliwu pa dzanja langa, ndi kumwetsa mitundu yonse, imene ndikutumizirako.

16. Ndipo adzamwa, nadzayenda dzandi dzandi, nadzacita misala, cifukwa ca lupanga limene Ine ndidzatumiza mwa iwo.

17. Ndipo ndinatenga cikho pa dzanja la Yehova, ndinamwetsa mitundu yonse, imene Yehova ananditumizirako;

18. Yerusalemu, ndi midzi ya Yuda, ndi mafumu ace omwe, ndi akuru ace, kuwayesa iwo bwinja, cizizwitso, cotsonyetsa, ndi citemberero; monga lero lino;

19. Farao mfumu ya ku Aigupto, ndi atumiki ace, ndi akuru ace, ndi anthu ace onse;

20. ndi anthu onse osanganizidwa, ndi mafumu onse a dziko la Uzi, ndi mafumu onse a dziko la Afilisti, ndi Asikeloni, ndi Gaza, ndi Ekroni, ndi otsala a Asdodi,

21. Edomu, ndi Moabu, ndi ana a Amoni,

22. ndi mafumu onse a Turo, ndi mafumu onse a Zidoni, ndi mafumu a cisumbu cimene ciri patsidya pa nyanja;

23. Dedani, ndi Tema, ndi Buzi, ndi onse amene ameta m'mbali mwa tsitsi;

24. ndi mafumu onse a Arabiya, ndi mafumu onse a anthu osanganizidwa okhala m'cipululu;

25. ndi mafumu onse a Zimiri, ndi mafumu onse a Elamu, ndi mafumu onse a Medi,

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 25