Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 23:13-26 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Ndipo ndinaona kupusa mwa aneneri a ku Samariya; anenera za Baala, nasokeretsa anthu anga Israyeli.

14. Mwa aneneri a ku Yerusalemu ndinaona cinthu coopsetsa; acita cigololo, ayenda monama, alimbitsa manja a ocita zoipa, ndipo palibe wobwerera kuleka zoipa zace; onse akhala kwa Ine ngati Sodomu, ndi okhalamo ace ngati Gomora.

15. Cifukwa cace Yehova wa makamu atero za aneneri: Taonani, ndidzadyetsa iwo cowawa, ndidzamwetsa iwo madzi andulu; pakuti kwa aneneri a ku Yerusalemu kuipitsa kwaturukira kunka ku dziko lonse.

16. Yehova wa makamu atero, Musamvere mau a aneneri amene anenera kwa inu; akuphunzitsani zacabe; anena masomphenya a mtima wao, si a m'kamwa mwa Yehova.

17. Anena cinenere kwa iwo akundinyoza Ine, ati Yehova, Mudzakhala ndi mtendere; ndipo kwa yense amene ayenda m'kuumirira kwa mtima wace amati, Palibe coipa cidzagwera inu.

18. Pakuti ndani waima m'upo wa Yehova, kuti aone namve mau ace? ndani wazindikira mau anga, nawamva?

19. Taonani, cimphepo ca Yehova, kupsa mtima kwace, kwaturuka, inde cimphepo cozungulira; cidzagwa pamutu pa woipa.

20. Mkwiyo wa Yehova sudzabwerera, mpaka atacita, mpaka atatha maganizo a mtima wace; masiku otsiriza mudzacidziwa bwino.

21. Sindinatuma aneneri awa, koma anathamanga; sindinanena ndi iwo, koma ananenera.

22. Koma akadaima m'upo wanga, akadamvetsa anthu anga mau anga, akadatembenuza iwo ku njira yao yoipa, ndi ku coipa ca nchito zao.

23. Kodi ndine Mulungu wa pafupi, ati Yehova, si Mulungu wa patari?

24. Kodi munthu angathe kubisala mobisika kuti ndisamuone iye? ati Yehova. Kodi Ine sindidzala kumwamba ndi dziko lapansi? ati Yehova.

25. Ndamva conena aneneri, amene anenera zonama m'dzina langa, kuti, Ndalota, ndalota.

26. Ici cidzakhala masiku angati m'mtima mwa aneneri amene anenera zonama; ndiwo aneneri a cinyengo ca mtima wao?

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 23