Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 21:1-4 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Mau amene anadza kwa Yeremiya kucokera kwa Yehova, pamene Zedekiya mfumu anatuma kwa iye Pasuri mwana wa Malikiya, ndi Zefaniya mwana wace wa Maseya wansembe, akati,

2. Titunsirenitu ife kwa Yehova; pakuti Nebukadirezara mfumu wa ku Babulo atithira ife nkhondo; kapena Yehova adzaticitira ife monga mwa nchito zace zolapitsa, kuti aticokere.

3. Ndipo Yeremiya anati kwa iwo, Muzitero kwa Zedekiya:

4. Yehova, Mulungu wa Israyeli atero, Taonani, ndidzabweza zida za nkhondo zimene ziri m'manja anu, zimene mumenyana nazo ndi mfumu ya ku Babulo, ndi Akasidi akuzinga inu, kunja kwa malinga, ndipo ndidzazisonkhanitsa pakati pa mudzi uwu.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 21