Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 20:6-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Ndipo iwe, Pasuri, ndi onse okhala m'nyumba mwako mudzanka kundende; ndipo udzafika ku Babulo, ndi pamenepo udzafa, ndi pamenepo udzaikidwa, iwe, ndi mabwenzi ako onse, amene unawanenera mabodza.

7. Yehova, mwandikopa ine, ndipo ndinakopedwa; muli ndi mphamvu koposa ine, ndipo mwalakika; ine ndikhala coseketsa dzuwa lonse, lonse andiseka.

8. Pakuti pali ponse ndinena, ndipfuula; ndipfuula, Ciwawa ndi cofunkha; pakuti mau a Mulungu ayesedwa kwa ine citonzo, ndi coseketsa, dzuwa lonse.

9. Ndipo ngati nditi, Sindidzamchula Iye, sindidzanenanso m'dzina lace, pamenepo m'mtima mwanga muli ngati moto wotentha wotsekedwa m'mafupa anga, ndipo ndalema ndi kupirira, sindingathe kupiriranso.

10. Pakuti ndamva kugogodera kwa ambiri, mantha pozungulira ponse. Neneza, ndipo tidzamneneza iye, ati atsamwali anga onse, amene ayang'anira kutsimphina kwanga; kapena adzakopedwa, ndipo ife tidzamlaka iye, ndipo tidzambwezera cilango.

11. Koma Yehova ali ndi ine ngati wamphamvu ndi woopsya; cifukwa cace ondisautsa adzapunthwa, sadzandilala; adzakhala ndi manyazi ambiri, cifukwa sanacita canzeru, ngakhale ndi kunyazitsa kwamuyaya kumene sikudzaiwalika.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 20