Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 2:3-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Israyeli anali wopatulikira Yehova, zipatso zoundukula za zopindula zace; onse amene adzamudya iye adzayesedwa oparamula; coipa cidzawagwera, ati Yehova.

4. Tamvani mau a Yehova, iwe nyumba ya Yakobo, ndi inu mabanja onse a nyumba ya Israyeli;

5. atero Yehova, Atate anu apeza cosalungama canji mwa Ine, kuti andicokera kunka kutari, natsata zacabe, nasanduka acabe?

6. Osati, Ali kuti Yehova amene anatikweza kucokera ku dziko la Aigupto, natitsogolera m'cipululu, m'dziko loti se ndi la maenje, m'dziko la cirala ndi la mthunzi wa imfa, m'dziko losapitamo anthu, losamangamo anthu?

7. Ndipo ndinakulowetsani m'dziko la minda, kuti mudye zipatso zace, ndi zabwino zace; koma pamene munalowa, munaipitsa dziko langa, ndi kuyesa colandira canga conyansa.

8. Ansembe sanati, Ali kuti Yehova? ndi iwo amene agwira malamulo sandidziwa Ine; ndi abusa omwe anandilakwira Ine, ndi aneneri ananenera mwa Baala, natsata zinthu zosapindula.

9. Cifukwa cace ndidzatsutsananso nanu, ati Yehova, ndi ana a ana anu ndidzatsutsana nao.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 2