Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 19:10-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Pamenepo uziphwanya nsupa pamaso pa anthu otsagana ndi iwe,

11. nuziti kwa iwo, Yehova wa makamu atero: Comweco ndidzaphwanya anthu awa ndi mudzi uwu, monga aphwanya mbiya ya woumba, imene sangathe kulumbanso, ndipo adzaika maliro m'Tofeti, mpaka mulibe malo akuikamo.

12. Ndidzatero ndi malo ano, ati Yehova, ndi okhalamo, kusanduliza mudzi uwu ngati Tofeti;

13. ndi nyumba za Yerusalemu, ndi nyumba za mafumu a Yuda, zimene ziipitsidwa, zidzanga malo a Tofeti, ndizo nyumba zonse anafukizira khamu lonse la kumwamba pa matsindwi ao, ndi kuithirira milungu yina nsembe zothira.

14. Pamenepo Yeremiya anadza kucokera ku Tofeti, kumene Yehova anamtuma iye kuti anenere; ndipo anaima m'bwalo la nyumba ya Yehova, nati kwa anthu onse:

15. Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli atero, Taonani, ndidzatengera mudzi uwu ndi midzi yace yonse coipa conse cimene ndaunenera; cifukwa anaumitsa khosi lao, kuti asamve mau anga.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 19