Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 19:1-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Atero Yehova, Pita, nugule nsupa ya woumba, nutenge akuru a anthu, ndi akuru a ansembe;

2. nuturukire ku cigwa ca mwana wace wa Hinomu, cimene ciri pa khomo la cipata ca mapale, nulalikire kumeneko mau amene ndidzakuuza iwe;

3. nuti, Tamvani mau a Yehova, inu mafumu a Yuda, ndi okhala m'Yerusalemu; Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli atero, Taonani, ndidzatengera malo ano coipa, cimene ali yense adzacimva, makutu ace adzacita woo.

4. Cifukwa andisiya Ine, nayesa malo ano acilendo, nafukizira m'menemo milungu yina, imene sanaidziwa, iwowa, ndi makolo ao ndi mafumu a Yuda: nadzaza malo ano ndi mwazi wa osacimwa;

5. namanga misanje ya Baala, kuti apsereze ana ao m'menemo nsembe zopsereza za Baala, cimene sindinawauza, sindinacinena, sicinalowa m'mtima mwanga;

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 19