Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 18:20-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

20. Kodi coipa cibwezedwe pa cabwino? pakuti akumbira moyo wanga dzenje, Mukumbukire kuti ndinaima pamaso panu kuwanenera zabwino, kuwacotsera iwo ukali wanu.

21. Cifukwa cace mupereke ana ao kunjala, mupereke iwo ku mphamvu ya lupanga; akazi ao akhale opanda ana, ndi amasiye; amuna ao aphedwe ndi imfa, ndi anyamata ao apandidwe ndi lupanga kunkhondo.

22. Mpfuu umvekedwe m'nyumba zao, pamene muwatengera khamu la nkhondo dzidzidzi; pakuti akumba dzenje lakundigwira ine, anabisira mapazi anga misampha.

23. Koma, Yehova, mudziwa uphungu wao wonse wakundinenera ine kundipha ine; musakhulukire mphulupulu yao, musafafanize cimo lao pamaso panu; apunthwitsidwe pamaso panu; mucite nao m'nthawi ya mkwiyo wanu.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 18