Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 18:1-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Mau amene anadza kwa Yeremiya kucokera kwa Yehova, kuti,

2. Tauka, tatsikira ku nyumba ya woumba, pamenepo ndidzakumvetsa mau anga.

3. Ndipo ndinatsikira ku nyumba ya woumba, ndipo, taonani, anaumba nchito yace ndi njinga.

4. Ndipo pamene mbiya alikulumba ndi dothi inaonongeka m'dzanja la woumba, anaiumbanso mbiya yina, monga kunamkomera woumba kulumba.

5. Ndipo mau a Yehova anadza kwa ine, kuti,

6. Nyumba ya Israyeli inu, kodi sindingathe kucita ndi inu monga woumba uyu? ati Yehova. Taonani, monga dothi m'dzanja la woumba, momwemo inu m'dzanja langa, nyumba ya Israyeli.

7. Mphindi imene ndidzanena za mtundu wa anthu, kapena za ufumu, kuti ndizule ndi kupasula ndi kuononga;

8. ngati mtundu umene, ndaunenera, udzatembenuka kuleka coipa cao, ndidzaleka coipaco ndidati ndiwacitire.

9. Ndipo mphindi imene ndikanenera mtundu, ndi ufumu, kuti ndimangitse mudzi wace ndi kuuoka;

10. koma ukacita coipa pamaso panga, osamvera mau anga, pamenepo ndidzaleka cabwinoco, ndidati ndiwacitire.

11. Tsopano nenatu kwa anthu a Yuda, ndi kwa okhala m'Yerusalemu, kuti, Atero Yehova: Taonani, Ine ndipangira inu coipa, ndilingalira inu kanthu kakucitira inu coipa; mubwerere tsono inu nonse, yense ku njira yace yoipa, nimukonze njira zanu ndi macitidwe anu.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 18