Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 15:9-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Mkazi amene anabala asanu ndi awiri walefuka; wapereka moyo; dzuwa lace lalowa usana ulipobe; wanyazitsidwa, wathedwa nzeru; otsala ao ndidzapereka kulupanga pamaso pa adani ao, ati Yehova.

10. Kalanga ine, amai, pakuti mwandibala ine munthu wandeu, munthu wakutetana nalo dziko lonse lapansi! sindinakongoletsa paphindu, anthu sanandikongoletsa paphindu; koma iwo onse anditemberera.

11. Yehova anati, Ndithu ndidzakulimbitsira iwe zabwino; ndithu ndidzapembedzetsa mdani kwa iwe nthawi ya zoipa ndi nthawi yansautso.

12. Kodi angathe munthu kutyola citsulo, citsulo ca kumpoto, ndi mkuwa?

13. Cuma cako ndi zosungidwa zako ndidzazipereka zifunkhidwe kopanda mtengo wace, icico cidzakugwera cifukwa ca zocimwa zako zonse, m'malire ako onse.

14. Ndipo ndidzawapititsa iwo pamodzi ndi adani ako ku dziko limene sudziwa iwe; pakuti moto wayaka m'mkwiyo wanga, umene udzatentha inu.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 15