Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 15:11-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Yehova anati, Ndithu ndidzakulimbitsira iwe zabwino; ndithu ndidzapembedzetsa mdani kwa iwe nthawi ya zoipa ndi nthawi yansautso.

12. Kodi angathe munthu kutyola citsulo, citsulo ca kumpoto, ndi mkuwa?

13. Cuma cako ndi zosungidwa zako ndidzazipereka zifunkhidwe kopanda mtengo wace, icico cidzakugwera cifukwa ca zocimwa zako zonse, m'malire ako onse.

14. Ndipo ndidzawapititsa iwo pamodzi ndi adani ako ku dziko limene sudziwa iwe; pakuti moto wayaka m'mkwiyo wanga, umene udzatentha inu.

15. Inu Yehova, mudziwa; mundikumbukire ine, mundiyang'anire ine, mundibwezere cilango pa ondisautsa ine; musandicotse m'cipiriro canu; dziwani kuti cifukwa ca Inu ndanyozedwa.

16. Mau anu anapezeka, ndipo ndinawadya; mau anu anakhala kwa ine cikondwero ndi cisangalalo ca mtima wanga; pakuti ndachedwa dzina lanu, Yehova Mulungu wa makamu.

17. Sindinakhala m'msonkhano wa iwo amene asekera-sekera, ndi kusangalala; ndinakhala pandekha cifukwa ca dzanja lanu; pakuti mwandidzaza ndi mkwiyo.

18. Kupweteka kwanga kuti cipwetekere bwanji, ndi bala langa losapoleka, likana kupola? kodi mudzakhala kwa ine ngati kamtsinje konyenga, ngati madzi omwerera?

19. Cifukwa cace atero Yehova, Ukabwerera pamenepo ndidzakubwezanso, kuti uime pamaso panga; ndipo ukasiyanitsa ca mtengo wace ndi conyansa, udzakhala ngati m'kamwa mwanga; ndipo adzabwerera kwa iwe, koma sudzabwerera kwa iwo.

20. Ndidzakuyesa iwe linga lamkuwa la anthu awa; ndipe adzamenyana ndi iwe, koma iwo sadzakuposa iwe; pakuti Ine ndiri ndi iwe kuti ndikupulumutse ndi kukulanditsa iwe, ati Yehova.

21. Ndipo ndidzakulanditsa iwe m'dzanja la oipa, ndipo ndidzakuombola iwe m'dzanja la oopsya.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 15