Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 11:16-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Yehova anacha dzina lako, Mtengo waazitona wauwisi, wokoma wa zipatso zabwino; ndi mau a phokoso lalikuru wayatsa moto pamenepo, ndipo nthambi zace zatyoka.

17. Pakuti Yehova wa makamu, amene anakuoka iwe, wakunenera iwe coipa, cifukwa ca zoipa za nyumba ya Israyeli ndi nyumba ya Yuda, zimene anadzicitira okha pakuutsa mkwiyo wanga m'mene anafukizira Baala.

18. Ndipo Yehova anandidziwitsa, ndipo ndinadziwa; ndipo wandisonyeza ine macitidwe ao.

19. Koma ine ndinanga mwana wa nkhosa wofatsa wotengedwa kukaphedwa; ndipo sindinadziwa kuti anandicitira ine ciwembu, kuti, Tiononge mtengo ndi zipatso zace, timdule iye pa dziko la amoyo, kuti dzina lace lisakumbukikenso.

20. Koma, Yehova wa makamu, amene aweruza molungama, pamene ayesa imso ndi mtima, ndikuoneni Inu mulikuwabwezera cilango, pakuti kwa Inu ndaulula mlandu wanga.

21. Cifukwa cace atero Yehova za anthu a Anatoti, amene afuna moyo wanga, kuti, Usanenere m'dzina la Yehova, ungafe ndi mkono wathu;

22. cifukwa cace atero Yehova wa makamu, Taonani, ndidzalanga iwo; anyamata adzafa ndi lupanga; ana ao amuna ndi akazi adzafa ndi njala;

23. ndipo sadzakhala nao otsalira; pakuti ndidzatengera coipa pa anthu a ku Anatoti, caka ca kulangidwa kwao.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 11