Pakuti Yehova wa makamu, amene anakuoka iwe, wakunenera iwe coipa, cifukwa ca zoipa za nyumba ya Israyeli ndi nyumba ya Yuda, zimene anadzicitira okha pakuutsa mkwiyo wanga m'mene anafukizira Baala.