Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 10:18-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Pakuti atero Yehova, Taonani, ndidzaponya kunja okhala m'dziko ili tsopanoli, ndi kuwasautsa, kuti azindikire.

19. Tsoka ine, ndalaswa! bala langa lindipweteka; koma ine ndinati, Ndithu bvuto langa ndi ili, ndipirire nalo.

20. Hema wanga waonongeka, zingwe zanga zonse zaduka; ana anga aturuka mwa ine, palibe iwo; palibenso amene adzamanga hema wanga, kapena kucinga nsaru zanga,

21. Pakuti abusa apulukira, sanafunsire kwa Yehova; cifukwa cace sanapindula; zoweta zao zonse zabalalika.

22. Mbiri yamveka, taonani ikudza, ndi phokoso lalikuru lituruka m'dziko la kumpoto, likacititse midzi ya Yuda bwinja, ndi mbuto ya nkhandwe.

23. Inu Yehova, ndidziwa kuti njira ya munthu siri mwa iye mwini; sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ace.

24. Yehova, mundilangize, koma ndi ciweruzo; si m'mkwiyo wanu, mungandithe psiti.

25. Tsanulirani ukali wanu pa amitundu osakudziwani Inu, ndi pa mabanja osaitana dzina lanu; pakuti anadya Yakobo, inde, anamudya namutha, napasula mokhalamo mwace.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 10