Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 10:12-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Iye analenga dziko lapansi ndi mphamvu yace, nakhazikitsa dziko lapansi ndi nzeru yace, nayala thambo ndi kuzindikira kwace;

13. polankhula Iye, pali unyinji wa madzi m'mwamba, ndipo akweretsa nkhungu ku malekezero a dziko lapansi, alenga mphezi idzetse mvula, naturutsa mphepo m'zosungira zace.

14. Anthu onse ali opulukira ndi opanda nzeru; woyenga yense anyazitsidwa ndi fanizo lace losemasema; pakuti fanizo lace loyenga liri bodza, mulibe mpweya mwa iwo.

15. Ndiwo cabe, ndiwo ciphamaso; pa nthawi ya kulangidwa kwao adzatha.

16. Gawo la Yakobo silifanana ndi iwo; pakuti iye ndiye analenga zonse; Israyeli ndiye mtundu wa colowa cace; dzina lace ndi Yehova wa makamu.

17. Nyamula katundu wako, iwe wokhala m'linga.

18. Pakuti atero Yehova, Taonani, ndidzaponya kunja okhala m'dziko ili tsopanoli, ndi kuwasautsa, kuti azindikire.

19. Tsoka ine, ndalaswa! bala langa lindipweteka; koma ine ndinati, Ndithu bvuto langa ndi ili, ndipirire nalo.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 10