Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 10:1-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Tamvani mau amene Yehova anena kwa inu, nyumba ya Israyeli;

2. atero Yehova, a Musaphunzire njira ya amitundu, musaope zizindikiro za m'thambo; pakuti amitundu aziopa izo.

3. Pakuti miyambo ya anthu iri yacabe, pakuti wina adula mtengo m'nkhalango, nchito ya manja a mmisiri ndinkhwangwa.

4. Aukometsa ndi siliva ndi golidi; aucirikiza ndi misomali ndi nyundo, kuti usasunthike.

5. Mafanowa akunga mtengo wakanjedza, wosemasema, koma osalankhula; ayenera awanyamule, pakuti sangathe kuyenda. Musawaope; pakuti sangathe kucita coipa, mulibenso mwa iwo kucita cabwino.

6. Cifukwa palibe akunga Inu, Yehova; muli wamkuru, ndipo dzina lanu liri lalikuru ndi lamphamvu,

7. Wosaopa Inu ndani, Mfumu ya amitundu? pakuti kukuopani ndi kwanu; pakuti mwa anzeru onse a amitundu, ndi m'maufumu ao onse, mulibe akunga Inu.

8. Koma onse pamodzi apulukira ndi kupusa; mtengo ndiwo cilangizo, copanda pace.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 10